63 Ana a Merari analandira mwa maere monga mwa mabanja ao, motapa pa pfuko la Rubeni, ndi pa pfuko la Gadi, ndi pa pfuko la Zebuluni, midzi khumi ndi iwiri.
64 Ndipo ana a Israyeli anapatsa Alevi midzi ndi mabusa ao.
65 Ndipo anapatsa mwamaere, motapa pa pfuko la ana a Yuda, ndi pa pfuko la Simeoni, ndi pa pfuko la ana a Benjamini, midzi iyi yochulidwa maina ao.
66 Ndi mabanja ena a ana a Kohati anali nayo midzi ya malire ao, yotapa pa pfuko la Efraimu.
67 Ndipo anawapatsa midzi yopulumukiramo: Sekemu ndi mabusa ace ku mapiri a Efraimu, Gezeri ndi mabusa ace,
68 ndi Yokimeamu ndi mabusa ace, ndi Betihoroni ndi mabusa ace,
69 ndi Ayaloni ndi mabusa ace, ndi Gatirimoni ndi mabusa ace,