9 Comweco Hana anauka atadya m'Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wace pa mphuthu ya Kacisi wa Yehova.
10 Ndipo mkaziyo anali ndi mtima wowawa, napemphera kwa Yehova, naliratu misozi;
11 nalonjeza cowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukila ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wace, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pace.
12 Ndipo panali, m'mene iye analikupempherabe pamaso pa Yehova, Eli anapenyerera pakamwa pace.
13 Koma Hana ananena mu mtima; milomo yace inatukula, koma mau ace sanamveka; cifukwa cace Eli anamuyesa woledzera.
14 Ndipo Eli anati kwa iye, Udzaleka liti kuledzera? cotsa vinyo wako.
15 Ndipo Hana anayankha, nati, Iai, mbuyanga. Ine ndiri mkazi wa mtima wacisoni; sindinamwa vinyo kapena cakumwa cowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova.