17 Ndipo Samueli anaitana anthu onse asonkhane kwa Yehova ku Mizipa;
18 nanena ndi ana a Israyeli, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli kuti, Ine ndinaturutsa Israyeli m'Aigupto, ndipo ndinakupulumutsani m'manja a Aaigupto, ndi m'manja a maufumu onse anakusautsani;
19 koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Cifukwa cace tsono mudzionetse pamaso pa Mulungu mafuko mafuko, ndi magulu magulu.
20 Comweco Samueli anayandikizitsa mafuko onse a Israyeli, ndipo pfuko la Benjamini linasankhidwa.
21 Nayandikizitsa pfuko la Benjamini, banja ndi banja, ndipo banja la Amatiri linasankhidwa; nasankhidwa Sauli mwana wa Kisi. Koma pamene anamfuna, anapeza palibe.
22 Cifukwa cace anaonjeza kufunsa Yehova, Watsala wina kodi woyenera kubwera kuno? Ndipo Yehova anati, Onani, alikubisala pakati pa akatundu.
23 Ndipo anathamanga, namtenga komweko; ndipo iye pamene anaima pakati pa anthuwo, anali wamtali koposa anthu onse anamlekeza m'cifuwa.