5 Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisrayeli, anali nao magareta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi cimodzi, ndi anthu akucuruka monga mcenga wa pa dooko la nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni.
6 Pamene anthu a Israyeli anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.
7 Ndipo Ahebri ena anaoloka Yordano nafika ku dziko la Gadi ndi Gileadi; koma Sauli akali ku Giligala, ndipo anthu onse anamtsata ndi kunthunthumira.
8 Ndipo iye anatsotsa masiku asanu ndi awiri, monga nthawi anampanga Samueli; koma Samueli sanafika ku Giligala, ndipo anthu anabalalika namsiya Sauli.
9 Pamenepo Sauli anati, Andipatsire kuno nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika. Ndipo iye anapereka nsembe yopserezayo.
10 Ndipo kunali kuti pakutsiriza iye kupereka nsembe yopserezayo, pomwepo, onani, Samueli anafika. Ndipo Sauli anamcingamira kukamlankhula iye.
11 Ndipo Samueli anati, Mwacitanji? Nati Sauli, Cifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafika masiku aja tinapangana, ndi kuti Afilisti anasonkhana ku Mikimasi;