23 Comweco Yehova anapulumutsa Israyeli tsiku lija; ndipo nkhondo inapitirira pa Betaveni.
24 Ndipo Aisrayeli anasauka tsiku lija; pakuti Sauli anawalumbirira, kuti, Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere cilango adani anga. Motero anthu onse anakhala opanda kudya.
25 Ndipo anthu onsewo analowa munkhalango, panali uci pansi.
26 Ndipo pakufika anthuwo m'nkhalangomo, onani, madzi a uci anacuruka; koma panalibe munthu mmodzi anaika dzanja lace pakamwa, pakuti anthuwo anaopa tembererolo.
27 Koma Jonatani sanamva m'mene atate wace analumbirira anthu; cifukwa cace iye ana tam balitsa ndodo ya m'dzanja lace, naitosa m'cisa ca uci, naika dzanja lace pakamwa pace; ndipo m'maso mwace munayera.
28 Ndipo wina wa anthuwo anayankha, nati, Atate wanu analangiza anthu kolimba ndi lumbiro, ndi kuti, Wotembereredwa iye wakudya lero cakudya. Ndipo anthuwo analema.
29 Ndipo Jonatani anati, Atate wanga wabvuta dziko; onani m'maso mwanga mwayera, cifukwa ndinalawako pang'ono uciwu.