12 Ndipo Samueli analawirira m'mawa kuti akakomane ndi Sauli; ndipo munthu anamuuza Samueli kuti, Sauli anafika ku Karimeli, ndipo taonani, anaimika cikumbutso cace, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala.
13 Ndipo Samueli anadza kwa Sauli; ndipo Sauli anati kwa iye, Yehova akudalitseni; ine ndinacita lamulo la Yehova.
14 Ndipo Samueli anati, Koma tsono kulirako kwa nkhosa ndirikumva m'makutu anga, ndi kulirako kwa ng'ombe ndirikumva, nciani?
15 Ndipo Sauli anati, Anazitenga kwa Aamaleki; pakuti anthu anasunga nkhosa zokometsetsa ndi ng'ombe, kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu; koma zina tinaziononga konse konse.
16 Pomwepo Samueli ananena ndi Sauli, Imani, ndidzakudziwitsani cimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.
17 Nati Samueli, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwa mutu wa mafuko a Israyeli? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israyeli,
18 Ndipo Yehova anakutumani ulendo, kuti, Muka, nuononge konse konse Aamaleki akucita zoipawo, nuponyane nao kufikira utawatha.