27 Ndipo pakupotoloka Samueli kuti acoke, iye anagwira cilezi ca mwinjiro wace, ndipo cinang'ambika.
28 Ndipo Samueli ananena naye, Yehova anang'amba ufumu wa Israyeli lero kuucotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.
29 Ndiponso Wamphamvu wa Israyeli sanama kapena kulapa; popeza iye sali munthu kuti akalapa.
30 Pomwepo iye anati, Ndinacimwa, koma mundicitire ulemu tsopano pamaso pa akuru a anthu anga, ndi pamaso pa Israyeli, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu.
31 Comweco Samueli anabwerera natsata Sauli; ndi Sauli analambira Yehova.
32 Ndipo Samueli anati, Bwerani naye kwa ine kuno Agagi mfumu ya Aamaleki. Ndipo Agagi anabwera kwa iye mokondwera. Nati Agagi, Zoonadi kuwawa kwa imfa kunapitirira.
33 Ndipo Samueli anati, Monga lupanga lako linacititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samueli anamdula Agagi nthuli nthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.