3 Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Jonatani asadziwe ici, kuti angamve cisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazilimodzi.
4 Ndipo Jonatani anati kwa Davide, Ciri conse mtima wako unena, ndidzakucitira.
5 Nati Davide kwa Jonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lacitatu madzulo ace.
6 Atate wako akandifuna pang'ono ponse, unene kuti, Davide anandiumirira ndimlole athamangire kwao ku Betelehemu, pakuti kumeneko kuli nsembe ya pacaka ya banja lao lonse.
7 Tsono akati, Cabwino; kapolo wako adzakhala ndi mtendere; koma akapsa mtima, uzindikirepo kuti anatsimikiza mtima kundicitira coipa.
8 Cifukwa cace ucitire kapolo wako zokoma mtima; popeza wamcititsa kapolo wako kupangana nawe pangano la kwa Yehova; koma ngati mwa ine muli coipa ciri conse, undiphe wekha; udzapita nane bwanji kwa atate wako?
9 Ndipo Jonatani anati, lai ndi pang'ono ponse; ine ndikadziwa konse kuti atate wanga anatsimikiza mtima kukucitira coipa, sindidzadziwitsa iwe kodi?