5 Ndipo kunali m'tsogolo mwace kuti a mtima wa Davide unamtsutsa cifukwa adadula mkawo wa mwinjiro wa Sauli.
6 Nati kwa anyamata ace, Mulungu andiletse kucitira ici mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.
7 Comweco Davide analetsa anyamata ace ndi mau awa, osawaloleza kuukira Sauli. Ndipo Sauli ananyamuka, naturuka m'phangamo, namuka njira yace.
8 Bwino lace Davide yemwe ananyamuka, naturuka m'phangamo, napfuulira Sauli, nati, Mbuye wanga, mfumu. Ndipo pakuceuka Sauli, Davide anaweramira nkhope yace pansi, namgwadira.
9 Davide nanena ndi Sauli, Bwanji mulikusamalira mau a anthu akuti, Onani, Davide afuna kukucitirani coipa.
10 Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, Sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; cifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.
11 Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe coipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakucimwirani, cinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire,