1 Ndipo Davide ananena mumtima mwace, Tsiku tina Sauli adzandipha; palibe cina condikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Sauli adzakhala kakasi cifukwa ca ine, osandifunanso m'malire onse a Israyeli, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lace.
2 Ndipo Davide ananyamuka, naoloka pamodzi ndi anthu mazana asanu ndi limodzi amene anali naye, nafika kwa Akisi mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati.
3 Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ace, munthu yense ndi a pabanja pace, inde Davide ndi akazi ace awiri, Ahinoamu wa ku Jezreeli, ndi Abigayeli wa ku Karimeli, mkazi wa Nabala.
4 Ndipo anauza Sauli kuti Davide anathawira ku Gati; ndipo iye sanamfunanso.
5 Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kumiraga, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji m'mudzi wacifumu pamodzi ndi inu?
6 Ndipo Akisi anampatsa Zikilaga tsiku lomweli; cifukwa cace Zikilaga ndi wa mafumu a Yuda kufikira lero lomwe.