8 Ndipo Davide ndi anthu ace anakwera, nathira nkhondo yobvumbulukira pa Agesuri, ndi Agirezi, ndi Aamaleki; pakuti awa ndiwo anthu akale a m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Aigupto.
9 Ndipo Davide anapasula dzikolo, sanasunga ndi moyo mwamuna kapena wamkazi; natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi aburu, ndi ngamila, ndi zobvala; nabwera nafika kwa Akisi.
10 Ndipo Akisi anati, Wapooyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameli, ndi a kumwera kwa Akeni.
11 Ndipo Davide sadasunga wamoyo mwamuna kapena mkazi, kubwera nao ku Gati; popeza adati, Kuti angatiulule, ndi kuti, Davide anatero, ndi makhalidwe ace ndi otere, masiku onse akukhala ku dziko la Afilisti.
12 Ndipo Akisi anakhulupirira Davide, nati Anadziipitsa ndithu pakati pa anthu a Israyeli, cifukwa cace iye adzakhala mnyamata wanga cikhalire.