14 Ndipo midzi ya Israyeli imene Afilisti adailanda kale inabwezedwa kwa Aisrayeli, kuyambira ku Ekroni kufikira ku Gati; ndi Aisrayeli analanditsa miraga yao m'manja a Afilisti. Ndipo pakati pa Aisrayeli ndi Aamori panali mtendere;
15 ndipo Samueli anaweruza Israyeli masiku onse a moyo wace.
16 Ndipo anayenda cozungulira caka ndi caka ku Beteli, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israyeli m'malo onse amenewa.
17 Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yace inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israyeli; namangapo guwa la nsembe la Yehova.