1 Ndipo kunali, pamene Samueli anakalamba, anaika ana ace amuna akhale oweruza a Israyeli.
2 Dzina la mwana wace woyamba ndiye Yoeli, ndi dzina la waciwiri ndiye Abiya; ndiwo oweruza a ku Beereseba.
3 Ndipo ana ace sanatsanza makhalidwe ace, koma anapambukira ku cisiriro, nalandira cokometsera mlandu, naipitsa kuweruza.
4 Pamenepo akuru onse a Israyeli anasonkhana, nadza kwa Samueli ku Rama;
5 nanena naye, Taonani, mwakalamba, ndipo ana anu satsanza makhalidwe anu; tsono, mutilongere mfumu kuti ikatiweruze, monga umo mucitidwa m'mitundu yonse ya anthu.
6 Koma cimeneci sicinakondweretsa Samueli, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samueli anapemphera kwa Yehova.
7 Ndipo Yehova ananena ndi Samueli, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.