18 Cifukwa cace Yehova anakwiya naye Israyeli kwakukuru, nawacotsa pamaso pace osatsala mmodzi, koma pfuko la Yudalokha.
19 Yudansosanasunga malamulo a Yehova Mulungu wao, koma anayenda m'malemba a Israyeli amene adawaika.
20 Ndipo Yehova anakaniza mbumba yonse ya Israyeli, nawazunza, nawapereka m'dzanja la ofunkha, mpaka anawataya pamaso pace.
21 Pakuti anang'amba Israyeli, kumcotsa ku nyumba ya Davide; ndipo anamlonga mfumu Yerobiamu mwana wa Nebati; Yerobiamu naingitsa Israyeli asatsate Yehova, nawalakwitsa kulakwa kwakukuru.
22 Nayenda ana a Israyeli m'zolakwa zonse za Yerobiamu, zimene anazicita osazileka;
23 mpaka Yehova adacotsa Israyeli pamaso pace, monga adanena mwa dzanja la atumiki ace onse aneneriwo. Momwemo Israyeli anacotsedwa m'dziko lao kumka nao ku Asuri mpaka lero lino.
24 Ndipo mfumu ya Asuri anabwera nao anthu ocokera ku Babulo, ndi ku Kuta, ndi ku Ava, ndi ku Hamati, ndi ku Safaravaimu, nawakhalitsa m'midzi ya Samariya, m'malo mwa ana a Israyeli; nakhala iwo eni ace a Samariya, nakhala m'midzi mwace.