1 Ndipo Yehosafati mfumu ya Yuda anabwerera ku nyumba yace ku Yerusalemu mumtendere.
2 Naturuka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza oipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Cifukwa ca ici ukugwerani mkwiyo wocokera kwa Yehova.
3 Koma zapezeka zokoma mwa inu, popeza mwazicotsa zifanizo m'dzikomo, mwaluniikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu.
4 Ndipo Yehosafati anakhala ku Yerusalemu, naturukiranso mwa anthu kuyambira ku Beereseba kufikira ku mapiri a Efraimu; nawabweza atsatenso Yehova Mulungu wa makolo ao.
5 Naika oweruza m'dziko, m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda, m'mudzi m'mudzi;
6 nati kwa oweruza, Khalani maso umo mucitira; pakuti simuweruzira anthu koma Yehova; ndipo ali nanu Iyeyu pakuweruza mlandu.
7 Ndipo tsono, kuopa Yehova kukhale pa inu, musamalire ndi kucita; pakuti palibe cosalungama kwa Yehova Mulungu wathu, kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu, kapena kulandira mphatso.