1 Ndipo anthu onse Ayuda anatenga Uziya, ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wace Amaziya.
2 Iye anamanga Eloti, naubweza kwa Yuda, mfumu itagona ndi makolo ace.
3 Uziya anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu ziwiri; ndi dzina la mace ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.
4 Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazicita atate wace Amaziya.
5 Ndipo iye anali munthu wakufuna Mulungu masiku a Zekariya, ndiye wozindikira masomphenya a Mulungu; ndipo masiku akufunira Yehova iye, Mulungu anamlemereza;