17 Pakuti Aedomu anadzanso, nakantha Yuda, natenga andende.
18 Afilisti omwe adagwa m'midzi ya kucidikha, ndi ya kumwela kwa Yuda, nalanda Betisemesi, ndi Azaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi miraga yace, ndi Timna ndi miraga yace; nakhala iwo komweko.
19 Pakuti Yehova anacepetsa Yuda cifukwa ca Ahazi mfumu ya Israyeli; popeza iye anacita comasuka pakati pa Yuda, nalakwira Yehova kwambiri.
20 Ndipo Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri anadza kwa iye, namsautsa osamlimbikitsa.
21 Pakuti Ahazi analandako za m'nyumba ya Yehova ndi za m'nyumba ya mfumu, ndi ya akalonga, nazipereka kwa mfumu ya Asuri, osathandizidwa nazo.
22 Ndipo nthawi ya nsautso yace anaonjeza kulakwira Yehova, mfumu Ahazi yemweyo.
23 Popeza anaphera nsembe milungu ya Damasiko yomkantha, nati, Popeza milungu ya mafumu a Aramu iwathandiza, ndiiphere nsembe, indithandize inenso. Koma inamkhumudwitsa iye, ndi Aisrayeli onse.