1 Hezekiya analowa ufumu wace ali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la mace ndiye Abiya mwana wa Zekariya.
2 Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo monse adacitira Davide kholo lace.
3 Caka coyamba ca ufumu wace, mwezi woyamba, anatsegula pa makomo a nyumba ya Yehova, napakonzanso.
4 Nalowetsa ansembe ndi Alevi, nawasonkhanitsa pamalo poyera kum'mawa,
5 nanena nao, Ndimvereni, Alevi inu, dzipatuleni, nimupatule nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu, ndi kucotsa zoipsa m'malo opatulika.
6 Pakuti analakwa makolo athu, nacita coipa pamaso pa Yehova Mulungu wathu, namsiya, natembenuza nkhope zao osapenya cokhalamo Yehova, namfulatira.
7 Anatsekanso pa khomo la likole, nazima nyalizo, osafukizanso zonunkhira kapena kupereka nsembe zopsereza m'malo opatulika kwa Mulungu wa Israyeli.