1 Pamenepo Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, m'phiri la Moriya, kumene Mulungu anaonekera kwa Davide atate wace, pamalo pamene Davide anakonzeratu pa dwale la Orinani Myebusi.
2 Nayamba kumanga tsiku laciwiri la mwezi waciwiri, caka cacinai ca ufumu wace.
3 Ndipo maziko adawaika Solomo akumangapo nyumba ya Mulungu ndi awa: utali wace, kuyesa mikono monga mwa muyeso wakale, ndiwo mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri.
4 Ndi likole linali kukhomo kwa nyumba, m'litali mwace monga mwa kupingasa kwa nyumba munali mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace zana limodzi mphambu makumr awiri; ndipo analikuta m'katimo ndi golidi woona.