4 Ndi likole linali kukhomo kwa nyumba, m'litali mwace monga mwa kupingasa kwa nyumba munali mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace zana limodzi mphambu makumr awiri; ndipo analikuta m'katimo ndi golidi woona.
5 M'nyumba yaikuru tsono anacinga ndi mitengo yamlombwa, imene anaikuta ndi golidi wabwino, nalembapo ngati migwalangwa ndi maunyolo.
6 Ndipo anakuta nyumba ndi miyala ya mtengo wace; ndi golidi wace ndiye golidi wa Parivaimu.
7 Anamamatizanso kacisi, mitanda, ziundo, ndi makoma ace, ndi zitseko zace, ndi golidi; nalemba akerubi pamakoma.
8 Ndipo anamanga malo opatulikitsa, m'litali mwace monga mwa kupingasa kwa nyumba mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri; naikuta ndi golidi wabwino wakufikira matalente mazana asanu ndi limodzi.
9 Ndi kulemera kwace kwa misomali ndiko masekeli makumi asanu a golidi. Ndipo anazikuta ndi golidi zipinda zosanjikizana.
10 Ndipo m'malo opatulikitsa anapanga akerubi awiri, anacita osema, nawakuta ndi golidi.