1 Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi atatu mphambu cimodzi.
2 Nacita zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira za Davide kholo lace, osapambuka ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.
3 Pakuti atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lace; ndipo atakhala zaka khumi ndi cimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzicotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga,
4 Ndipo anthu anagumula maguwa a nsembe a Abaala pamaso pace; nawalikha mafano a dzuwa anakwezeka pamwamba pao; naphwanya zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga; nazipera, naziwaza pamanda pa iwo amene adaziphera nsembe.
5 Napsereza mafupa a ansembe pa maguwa a: nsembe ao, nayeretsa Yuda ndi Yerusalemu.
6 Nateronso m'midzi ya Manase, ndi Efraimu, ndi Simeoni, mpaka Nafitali, m'mabwinja mwao mozungulira.
7 Nagumula maguwa a nsembe, naperapera zifanizo ndi mafano osema, nalikha mafano a dzuwa onse m'dziko lonse la Israyeli, nabwerera kumka ku Yerusalemu.