23 Ndipo iye ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Muuze munthuyo anakutumizani kwa ine,
24 Atero Yehova, Taonani, ndifikitsira malo ano ndi anthu okhala m'mwemo coipa, ndico matemberero onse olembedwa m'buku adaliwerenga pamaso pa mfumu ya Yuda;
25 cifukwa anandisiya Ine, nafukizira milungu yina, kuti autse mkwiyo wanga ndi nchito zonse za manja ao; cifukwa cace ukali wanga utsanulidwa pamalo pano wosazimika.
26 Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero kwa iye, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Kunena za mau udawamva,
27 popeza mtima wako unali woolowa, ndipo wadzicepetsa pamaso pa Mulungu, pakumva mau ace otsutsana nao malo ano, ndi okhala m'mwemo, ndi kudzicepetsa pamaso panga, ndi kung'amba zobvala zako, ndi kulira pamaso panga; Inenso ndakumvera, ati Yehova.
28 Taona, ndidzakusonkhanitsa ku makolo ako, nudzaikidwa kumanda kwako mumtendere, ndi maso ako sadzapenya zoipa zonse ndidzafikitsira malo ano ndi okhala m'mwemo. Ndipo anambwezera mfumu mau.
29 Pamenepo mfumu inatumiza anthu, nisonkhanitsa akulu akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu.