6 Nateronso m'midzi ya Manase, ndi Efraimu, ndi Simeoni, mpaka Nafitali, m'mabwinja mwao mozungulira.
7 Nagumula maguwa a nsembe, naperapera zifanizo ndi mafano osema, nalikha mafano a dzuwa onse m'dziko lonse la Israyeli, nabwerera kumka ku Yerusalemu.
8 Atakhala mfumu tsono zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri, atayeretsa dziko ndi nyumbayi, anatuma safana mwana wa Azaliya, ndi Maseya kazembe wa mudzi, ndi Yona mwana wa Yoadazi wolemba mbiri, akonze nyumba ya Yehova Mulungu wace.
9 Ndipo anadza kwa Hilikiya wansembe wamkulu, napereka ndarama adabwera nazo ku nyumba ya Mulungu, zimene Alevi osunga pakhomo adasonkhanitsa kuzilandira ku dzanja la Manase ndi Efraimu, ndi kwa otsala onse a Israyeli, ndi kwa Yuda yense, ndi Benjamini, ndi kwa okhala m'Yerusalemu.
10 Ndipo anazipereka m'dzanja la anchito oikidwa ayang'anire nyumba ya Yehova; ndi iwo anazipereka kwa anchito akucita m'nyumba ya Yehova, kukonza ndi kulimbitsa nyumbayi;
11 anazipereka kwa amisiri a mitengo ndi omanga nyumba, agule miyala yosema, ndi mitengo ya mitanda yam'mwamba ndi yammunsi ya nyumbazi, adaziononga mafumu a Yuda.
12 Ndipo amunawo anacita nchitoyi mokhulupirika; ndi oikidwa awayang'anire ndiwo Yohati ndi Obadiya, Alevi, a ana a Merari; ndi Zekariya ndi Mesulamu, a ana a Akohati, kuifulumiza; ndi Alevi ena ali yense wa luso la zoyimbira,