1 Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Seba mbiri ya Solomo, anadza kumuyesera Solomo ndi miyambi yododometsa ku Yerusalemu, ndi ulendo waukuru, ndi ngamila zosenza zonunkhira, ndi golidi wocuruka, ndi timiyala ta mtengo wace; ndipo atafika kwa Solomo anakamba naye zonse za m'mtima mwace.
2 Ndipo Solomo anammasulira mau ace onse, panalibe kanthu kombisikira Solomo, kamene sanammasulira.
3 Ndipo mfumu yaikazi ya ku Seba ataiona nzeru ya Solomo, ndi nyumba adaimanga,
4 ndi zakudya za pa gome lace, ndi makhalidwe a anyamata ace, ndi maimiriridwe a atumiki ace, ndi mabvalidwe ao, ndi otenga zikho ace, ndi mabvalidwe ao, ndi makweredwe ace pokwera iye kumka ku nyumba ya Yehova, munalibenso moyo mwa iye.
5 Ndipo anati kwa mfumu, Inali yoona mbiri ija ndidaimva m'dziko langa, ya macitidwe anu, ndi ya nzeru zanu.
6 Koma sindinakhulupira mau ao mpaka ndinadza, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani anandifotokozera dera lina lokha la nzeru zanu zocuruka; mwa, onjezatu pa mbiri ndidaimva.