1 Ndipo kunali munthu ku Kaisareya, dzina lace Komeliyo, kenturiyo wa gulu lochedwa la Italiya,
2 ndiye munthu wopembedza, ndi wakuopa Mulungu ndi banja lace lonse, amene anapatsa anthu zacifundo zambiri, napemphera Mulungu kosaleka.
3 Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lacisanu ndi cinai la usana, nanena naye, Komeliyo.
4 Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nciani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zacifundo zako zinakwera zikhala cikumbutso pamaso pa Mulungu.