15 Ndipo mau anamdzeranso nthawi yaciwiri, Cimene Mulungu anayeretsa, usaciyesa cinthu wamba.
16 Ndipo cinacitika katatu ici; ndipo pomwepo cotengeraco cinatengedwa kunka kumwamba.
17 Ndipo pokayika-kayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti ciani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Komeliyo, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pa cipata,
18 ndipo anaitana nafunsa ngati Simoni, wochedwanso Petro, acerezedwako.
19 Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu ananena naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe.
20 Komatu tauka, nutsike, ndipo upite nao, wosakayika-kayika; pakuti ndawatuma ndine.
21 Ndipo Petro anatsikira kwa anthuwo, nati, Taonani, ine ndine amene mumfuna; cifukwa cace mwadzera nciani?