31 nati Komeliyo, lamveka pemphero lako, ndi zopereka zacifundo zako zakumbukika pamaso pa Mulungu.
32 Cifukwa cace tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni amene anenedwanso Petro; amene acerezedwa m'nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, m'mbali mwa nyanja.
33 Pamenepo ndinatumiza kwa inu osacedwa; ndipo mwacita bwino mwadza kuno, Cifukwa cace taonani tiri tonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.
34 Ndipo Petro anatsegula pakamwa pace, nati:Zoona ndizinkidira kuti Mulungu alibe tsankhu;
35 koma m'mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakucita cilungamo alandiridwa naye.
36 Mau amene anatumiza kwa ana a Israyeli, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Kristu (ndiye Ambuye wa onse)
37 mauwo muwadziwa inu, adadzawo ku Yudeya lonse, akuyamba ku Galileya, ndi ubatizo umene Yohane anaulalikira;