4 Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nciani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zacifundo zako zinakwera zikhala cikumbutso pamaso pa Mulungu.
5 Ndipo tsopano tumiza amuna ku Y opa, aitane munthu Simoni, wochedwanso Petro;
6 acerezedwa iye ndi wina Simoni wofufuta zikopa, nyumba yace iri m'mbali mwa nyanja.
7 Ndipo m'mene atacoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ace awiri, ndi msilikari wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka;
8 ndipo m'mene adawafotokozerazonse, anawatuma ku Yopa.
9 Koma m'mawa mwace, pokhala paulendo pao iwowa, m'mene anayandikira mudzi, Petro anakwera pachindwi kukapemphera, ngati pa ora lacisanu ndi cimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya;
10 koma m'mene analikumkonzera cakudya kudamgwera ngati kukomoka;