41 si kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, 1 ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atauka iye kwa akufa.
42 Ndipo 2 anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo ticite umboni kuti 3 Uyu ndiye amene aikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa.
43 4 Ameneyu aneneri onse amcitira umboni, kuti onse akumkhulupirira iye adzalandira cikhululukiro ca macimo ao, mwa dzina lace.
44 Petro ali cilankhulire, 5 Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo.
45 Ndipo 6 anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, cifukwa pa 7 amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.
46 Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha,
47 Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera 8 ngatinso ife?