5 Ndinali ine m'mudzi wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, cotengera cirikutsika, ngati cinsaru cacikuru cogwiridwa pa ngondya zace zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo cinadza pali ine;
6 cimeneco ndidacipenyetsetsa ndinacilingirira, ndipo ndinaona nyama za miyendo inai za padziko ndi zirombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga.
7 Ndipo ndinamvanso mau akunena ndi ine, Tauka Petro; ipha, nudye.
8 Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m'kamwa mwanga ndi kale lonse.
9 Koma mau anayankha nthawi yaciwiri oturuka m'mwamba, Cimene Mulungu anaciyeretsa, usaciyesera cinthu wamba.
10 Ndipo ici cinacitika katatu; ndipo zinakwezekanso zonse kumwamba.
11 Ndipo taonani, pomwepo amuna atatu anaima pa khomo la nyumba m'mene munali ife, anatumidwa kwa ine ocokera ku Kaisareya.