13 Koma wansembe wa Zeu wa kumaso kwa mudzi, anadza nazo ng'ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi makamu.
14 Pamene anamva atumwi Paulo ndi Bamaba, anang'amba zopfunda zao, natumphira m'khamu,
15 napfuula Dati, Anthuni, bwanji mucita zimenezi? ifenso tiri anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zacabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse ziri momwemo:
16 m'mibadwo, yakale iye adaleka mitundu yonse iyende m'njira mwao.
17 Koma sanadzisiyira iye mwini wopanda umboni, popeza anacita zabwino, nakupatsani inu zocokera kumwamba mvulaodi nyengoza zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi cakudya ndicikondwero.
18 Pakunena izo, anabvutika pakuletsa makamu kuti asapereke nsembe kwa iwo.
19 Ndipo anafika kumeneko Ayuda kucokera ku Antiokeya ndi Ikoniyo; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulomiyala, namguzira kunja kwa mudzi; namuyesa kuti wafa.