1 Ndipo anafikanso ku Derbe ndi Lustra; ndipo taonani, panali wophunzira wina pamenepo, dzina lace Timoteo, amace ndiye Myuda wokhulupira; koma atate wace ndiye Mhelene.
2 Ameneyo anamcitira umboni wabwino abale a ku Lustra ndi Ikoniyo.
3 Iyeyo Paulo anafuna kuti amuke naye, ndipo anamtenga, namdula, cifukwa ca Ayuda amene anakhala m'maikomo; pakuti onse anadziwa kuti atate wace anali Mhelene.
4 Pamene anapita kupyola pamidzi, anapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene analamulira atumwi ndi akuru a pa Yerusalemu.