1 Zitapita izi anacoka ku Atene, nadza ku Korinto.
2 Ndipo anapeza Myuda wina dzina lace Akula, pfuko lace la ku Ponto, atacoka catsopano ku Italiya, pamodzi ndi mkazi wace Priskila, cifukwa Klaudiyo analamulira Ayuda onse acoke m'Roma; ndipo Pauloanadza kwa iwo:
3 ndipo popeza anali wa nchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira nchito; pakuti nchito yao inali yakusoka mahema.
4 Ndipo anafotokozera m'sunagogemasabata onse, nakopa Ayuda ndi Ahelene.