1 Ndipo pakufika tsiku la Penteskoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi.
2 Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ocokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo.
3 Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekha wayekha.
4 Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
5 Koma anali m'Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ocokera ku mtundu uli wonse pansi pa thambo.
6 Koma pocitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula m'cilankhulidwe cace ca iye yekha.