3 Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekha wayekha.
4 Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
5 Koma anali m'Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ocokera ku mtundu uli wonse pansi pa thambo.
6 Koma pocitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula m'cilankhulidwe cace ca iye yekha.
7 Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi?
8 ndipo nanga ife timva bwanji, yense m'cilankhulidwe cathu cimene tinabadwa naco?
9 Aparti ndi Amedi, ndi Aelami, ndi iwo akukhala m'Mesopotamiya, m'Yudeya, ndiponso m'Kapadokiya, m'Ponto, ndi m'Asiya;