27 Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.
28 Tadzicenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Eklesia wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa iye yekha.
29 Ndidziwa ine kuti, nditacoka ine, adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo;
30 ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.
31 Cifukwa cace dikirani, nimukumbukile kuti zaka zitatu sindinaleka usiku ndi usana kucenjeza yense wa inu ndi misozi.
32 Ndipo tsopano ndikuikizani kwa Mulungu, ndi kwa mau a cisomo cace, cimene ciri ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu colowa mwa onse oyeretsedwa.
33 Sindinasirira siliva, kapena golidi, kapena cobvala ca munthu ali yense.