14 Ndipo pokana iye kukopeka, tinaleka, ndi kuti, Kufuna kwa Ambuye kucitidwe.
15 Ndipo atapita masiku awa tinakonza akatundu athu, ntikwera ku Yerusalemu.
16 Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kaisareya, natenganso wina Mnaso wa ku Kupro, wophunzira wakale, amene adzaticereza.
17 Ndipo pofika ife ku Yerusalemu, abale anatilandira mokondwera.
18 Ndipo m'mawa mwace Paulo analowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse anali pomwepo.
19 Ndipo atawalankhula iwo, anawafotokozera cimodzi cimodzi zimene Mulungu anacita kwa amitundu mwa utumiki wace.
20 Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupira; ndipo ali naco cangu onsewa, ca pa cilamulo;