18 ndipo ndinamuona iye, nanena nane, Fulumira, turuka msanga m'Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine.
19 Ndipo ndinati ine, Ambuye, adziwa iwo okha kuti ndinali kuika m'ndende ndi kuwapanda m'masunagoge onse iwo akukhulupirira Inu;
20 ndipo pamene anakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndemwe ndinalikuimirirako, ndi kubvomerezana nao, ndi kusunga Zoobvala za iwo amene anamupha iye.
21 Ndipo anati kwa ine, Pita; cifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.
22 Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Acoke pa dziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.
23 Ndipo pakupfuula iwo, ndi kutaya zobvala zao, ndi kuwaza pfumbi mumlengalenga,
24 kapitao wamkuru analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe cifukwa cace nciani kuti ampfuulira comweco.