22 Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Acoke pa dziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.
23 Ndipo pakupfuula iwo, ndi kutaya zobvala zao, ndi kuwaza pfumbi mumlengalenga,
24 kapitao wamkuru analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe cifukwa cace nciani kuti ampfuulira comweco.
25 Ndipo m'mene anammanga iye ndi nsingazo, Paulo anati kwa kenturiyo wakuimirirako, Kodinkuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, mlandu wace wosamveka?
26 Ndipo pakumva ici kenturiyoyo, ananka kwa kapitao wamkuru, namuuza, nanena, Nciani ici uti ucite? pakuti munthuyo ndiye Mroma.
27 Ndipo kapitao wamkuruyo anadza, nati kwa iye, Ndiuze, iwe ndiwe Mroma kodi? Ndipo anati, Inde.
28 Ndipo kapitao wamkuru anayankha, Ine ndalandira ufulu umene ndi kuperekapo mtengo wace waukuru. Ndipo Paulo anati, Koma ine ndabadwa Mroma.