17 ndipo m'mene adaukweza, anacita nazo zothandizira, nakulunga ngalawa; ndipo pakuopa kuti angatayike pa Surti, anatsitsa matanga, natengedwa motero.
18 Ndipo pobvutika kwakukuru ndi namondweyo, m'mawa mwace anayamba kutaya akatundu;
19 ndipo tsiku lacitatu anataya ndi manja ao a iwo eni zipangizo za ngalawa.
20 Ndipo m'mene dzuwa kapena nyenyezi sizinatiwalira masiku ambiri, ndipo namondwe wosati wamng'ono anatigwera, ciyembekezo conse cakuti tipulumuke cidaticokera pomwepo.
21 Ndipo pamene atakhala nthawi yaikuru osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pao, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osacoka ku Krete, osadzitengera kuonongeka ndi kutayika kumene.
22 Koma tsopano ndikucenjezani mulimbike mtima; pakuti sadzatayika wamoyo mmodzi mwa inu, koma ngalawa ndiyo.
23 Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndiri wace, amenenso ndimtumikira,