1 Koma masiku awo, pakucurukitsa ophunzira, kunauka cidandaulo, Aheleniste kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa citumikiro ca tsiku ndi tsiku.
2 Ndipo khumi ndi awiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, Sikuyenera kuti ife tisiye mau a Mulungu ndi kutumikira podyerapo.
3 Cifukwa cace, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yahwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge nchito iyi.
4 Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau.