39 Ndipo Petro anayamuka, napita nao. M'mene anafikako, anapita naye ku cipinda ca pamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa maraya ndizobvala zimene Dorika adasoka, pamene anali nao pamodzi.
40 Koma Petro anawaturutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ace; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.
41 Ndipo Petro anamgwiradzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.
42 Ndipo kudadziwika ku Yopa konse: ndipo ambiri anakhulupirira Ambuye.
43 Ndipo kunali, kuti anakhala iye m'Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.