19 nati, Pali Mulungu wanga, kukhale kutali kwa ine kucita ici. Ngati ndidzamwa mwazi wa anthu awa? Akadataya moyo wao, inde akadataya moyo wao, pakukatenga madziwa. M'mwemo sanafuna kuwamwa. Izi anazicita atatu amphamvuwa.
20 Ndipo Abisai mbale wa Yoabu, ndiye wamkuru wa atatuwa; pakuti anasamulira mazana atatu mkondo wace, nawapha, namveka dzina pakati pa atatuwa.
21 Mwa atatuwa iye anali waulemu woposa awiriwa, nasanduka mkuru wao; koma sanafikana nao atatu oyamba aja.
22 Benaya mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi ya ku Kabzeeli, wocita zazikuru, anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Moabu; anatsikanso, napha mkango m'kati mwa dzenje nyengo ya cipale cofewa.
23 Anaphanso M-aigupto munthu wamkuru, msinkhu wace mikono isanu, ndi m'dzanja la M-aigupto munali mkondo ngati mtanda woombera nsaru; ndipo anamtsikira ndi ndodo, nakwatula mkondo m'dzanja la M-aigupto, namupha ndi mkondo wace womwe.
24 Izi anazicita Benaya mwana wa Yehoyada, namveka dzina mwa atatu amphamvuwo.
25 Taonani, anali wa ulemu woposa makumi atatuwo, koma sanafikana atatu oyamba aja; ndipo Davide anamuika mkuru wa olindirira ace.