11 Ndipo kudzacitika, atakwanira masiku ako kuti uzipita kukhala ndi makolo ako, ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, ndiye wa ana ako; ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wace.
12 Iye adzandimangira nyumba; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wacifumu wace kosatha.
13 Ndidzakhala atate wace, ndi iye adzakhala mwana wanga; ndipo sindidzamcotsera cifundo canga monga muja ndinacotsera iye amene anakhala usanakhale iwe;
14 koma ndidzamkhazikitsa m'nyumba mwanga, ndi m'ufumu wanga kosatha; ndi mpando wa cifumu wace udzakhazikika kosatha.
15 Monga mwa mau awa onse, ndi monga mwa masomphenya awa onse, momwemo Natani analankhula ndi Davide.
16 Pamenepo mfumu Davide analowa nakhala pamaso pa Yehova, nati, Ndine yani, Yehova Mulungu, ndi nyumba yanga njotani kuti mwandifikitsa mpaka pano?
17 Ndipo ici ncacing'ono pamaso panu, Mulungu, koma mwanena za nyumba ya mtumiki wanu nthawi yam'tsogolo ndithu, ndipo mwandiyesera ngati munthu womveka, Yehova Mulungu.