9 Ndipo pakumva Tou, mfumu ya ku Hamati, kuti Davide adakantha khamu lonse la Hadarezeri mfumu ya ku Zoba,
10 anatumiza Hadoramu mwana wace kwa Davide, kumlankhula ndi kumdalitsa, popeza adayambana ndi Hadarezeri, namkantha; pakuti Hadarezeri adacita nkhondo ndi Tou; ndipo anali nazo zipangizo za mitundu mitundu za golidi ndi siliva ndi mkuwa.
11 Izi zomwe mfumu Davide anazipatulira Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golidi adazitenga kwa amitundu onse, kwa Edomu, ndi kwa Moabu, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti, ndi kwa Amaleki.
12 Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu m'Cigwa ca Mcere zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu.
13 Ndipo anaika asilikari a boma m'Edomu; ndi Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kuli konse anamukako.
14 Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisrayeli onse, naweruza anthu ace onse, nawacitira cilungamo.
15 Ndipo Yoabu mwana wa Zeruya anayang'anira khamu la nkhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri.