11 Ndipo anthu otsala anawapereka m'dzanja la Abisai mbale wace; ndipo anadzinika avambane ndi ana a Amoni.
12 Ndipo anati, Akandilaka Aaramu, udzandilanditsa ndiwe; koma akakulaka ana a Amoni, ndidzakulanditsa ndine.
13 Limbika mtima, tilimbikire anthu athu, ndi midzi ya Mulungu wathu; ndipo Yehova acite comkomera.
14 Pamenepo Yoabu ndi anthu anali naye anayandikira pamaso pa Aaramu kulimbana nao, ndipo anawathawa.
15 Ndipo pakuona ana a Amoni kuti adathawa Aaramu, iwo omwe anathawa pamaso pa Abisai mbale wace, nalowa m'mudzi. Pamenepo Yoabu anadza ku Yerusalemu.
16 Ndipo pakuona Aaramu kuti Israyeli anawakantha, anatumiza mithenga, naturuka nao Aaramu akukhala tsidya lija la mtsinjewo; ndi Sofaki kazembe wa khamu la Hadarezeri anawatsogolera.
17 Ndipo anamuuza Davide; namemeza iye Aisrayeli onse, naoloka Yordano, nawadzera, nanika nkhondo ayambane nao. Atandandalitsa nkhondo Davide kuyambana ndi Aaramu, anaponyana naye.