3 Nakonzeratu Davide citsulo cocuruka ca misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wocuruka wosauyesa kulemera kwace;
4 ndi mitengo yamikungudza yosaiwerenga; pakuti Asidoni ndi Aturo anabwera nayo kwa Davide mitengo yamikungudza yocuruka,
5 Ndipo Davide anati, Solomo mwana wanga ndiye mnyamata ndi wosakwima, ndi nyumba imene adzaimangira Yehova ikhale yaikuru yopambana, yomveka ndi ya ulemerero mwa maiko onse; ndiikonzeretu mirimo. Momwemo Davide anakonzeratu mocuruka asanamwalire.
6 Pamenepo iye anaitana Solomo mwana wace, namlangiza ammangire Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.
7 Ndipo Davide anati kwa Solomo mwana wace, Kunena za ine, kumtima kwanga kudati, ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba.
8 Koma mau a Yehova anandidzera, kuti, Wakhetsa mwazi wocuruka, popeza wacita nkhondo zazikuru; sudzamangira dzina langa nyumba, popeza wakhetsa pansi mwazi wambiri pamaso panga;
9 taona, udzabala mwana, ndiye adzakhala munthu wa phe; ndipo nelidzampumulitsira adani ace onse pozungulirapo, pakuti dzina lace lidzakhala Solomo; ndipo ndidzapatsa Israyeli mtendere ndi bata masiku ace;