1 Ndipo magawidwe a ana a Aroni ndi awa. Ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.
2 Koma Nadabu ndi Abihu anafa, atate wao akali ndi moyo, opanda ana; momwemo Eleazara ndi ltamara anacita nchito ya nsembe.
3 Ndipo Davide pamodzi ndi Zadoki wa ana a Eleazara, ndi Ahimeleke wa ana a Itamara, anawagawa, monga mwa malongosoledwe ao m'utumiki wao.
4 Ndipo anapeza kuti amuna akuru a ana a Eleazara anacuruka, a ana a Itamara anacepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akuru a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu.
5 Ndipo anawagawa ndi maere, awa ndi aja; pakuti panali akalonga a malo opatulika, ndi akalonga a kwa Mulungu, a ana a Eleazara ndi a ana a Itamara omwe.