12 ndi cifaniziro ca zonse anali nazo mwa mzimu, ca mabwalo a nyumba ya Yehova, ndi ca zipinda zonse pozungulirapo, ca zosungiramo cuma za nyumba ya Mulungu, ndi ca zosungiramo cuma za zinthu zopatulika;
13 ndi ca magawidwe a ansembe ndi Alevi, ndi ca nchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova, ndi ca zipangizo za utumiki wa nyumba ya Yehova;
14 ca golidi woyesedwa kulemera kwace wa zipangizo zagolidi, wa zipangizo zonse za nchito ya mtundu uli wonse; ca siliva wa zipangizo zasiliva woyesedwa kulemera kwace, wa zipangizo za nchito ya mitundu mitundu;
15 mwa kulemera kwacenso ca zoikapo nyali zagolidi, ndi nyali zace zagolidi, mwa kulemera kwace ca coikapo nyali ciri conse, ndi nyali zace; ndi ca zoikapo nyali zasiliva, siliva woyesedwa kulemera kwace wa coikapo nyali ciri conse, ndi nyali zace, monga mwa coikapo nyali ciri conse;
16 ndi golidi woyesedwa kulemera kwace wa magome a makate woonekera, wa gome liri lonse; ndi siliva wa magome asiliva,
17 ndi mitengo, ndi mbale zowazira, ndi zikho za golidi woona, ndi ca mitsuko yace yagolidi, woyesedwa kulemera kwace mtsuko uli wonse; ndi ca mitsuko yasiliva woyesedwa kulemera kwace mtsuko uli wonse;
18 ndi ca guwa la nsembe lofukizapo la golidi woyengetsa woyesedwa kulemera kwace, ndi cifaniziro ca gareta wa akerubi agolidi akufunyulula mapiko ao ndi kuphimba likasa la cipangano la Yehova.