9 Ndipo iwe Solomo mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna iye udzampeza, koma ukamsiya iye adzakusiya kosatha.
10 Cenjera tsono, pakuti Yehova anakusankha iwe umange nyumba ya malo opatulika; limbika, nucite.
11 Pamenepo Davide anapatsa Solomo mwana wace cifaniziro ca likole la kacisi, ndi ca nyumba zace, ndi ca zosungiramo cuma zace, ndi ca zipinda zosanjikizana zace, ndi ca zipinda zace za m'katimo, ndi ca kacisi wotetezerapo;
12 ndi cifaniziro ca zonse anali nazo mwa mzimu, ca mabwalo a nyumba ya Yehova, ndi ca zipinda zonse pozungulirapo, ca zosungiramo cuma za nyumba ya Mulungu, ndi ca zosungiramo cuma za zinthu zopatulika;
13 ndi ca magawidwe a ansembe ndi Alevi, ndi ca nchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova, ndi ca zipangizo za utumiki wa nyumba ya Yehova;
14 ca golidi woyesedwa kulemera kwace wa zipangizo zagolidi, wa zipangizo zonse za nchito ya mtundu uli wonse; ca siliva wa zipangizo zasiliva woyesedwa kulemera kwace, wa zipangizo za nchito ya mitundu mitundu;
15 mwa kulemera kwacenso ca zoikapo nyali zagolidi, ndi nyali zace zagolidi, mwa kulemera kwace ca coikapo nyali ciri conse, ndi nyali zace; ndi ca zoikapo nyali zasiliva, siliva woyesedwa kulemera kwace wa coikapo nyali ciri conse, ndi nyali zace, monga mwa coikapo nyali ciri conse;